Isaiah 8:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndiye adzakhala ngati malo opatulika. Koma kwa anthu a ku Yuda ndi a ku Israele adzakhala ngati mwala wokhumudwitsa, ndiponso ngati thanthwe logwetsetsa. Kwa anthu a mu Yerusalemu, adzakhala ngati msampha ndi khwekhwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye adzakhala malo opatulika; koma mwala wophunthwitsa, ndi thanthwe lolakwitsa la nyumba zonse ziwiri za Israele, khwekhwe ndi msampha wa okhala m'Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo ndiye amene adzakhala malo opatulika; koma kwa anthu a ku Yuda ndi kwa anthu a ku Israeli adzakhala mwala wopunthwitsa, mwala umene umapunthwitsa anthu, thanthwe limene limagwetsa anthu. Ndipo kwa anthu a mu Yerusalemu adzakhala ngati msampha ndi khwekhwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Iye adzakhala malo opatulika; koma mwala wopunthwitsa, ndi thanthwe lolakwitsa la nyumba zonse ziwiri za Israyeli, khwekhwe ndi msampha wa okhala m'Yerusalemu.