Isaiah 8:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthu akakuuzani kuti, “Kafunseni kwa olankhula ndi mizimu ndi kwa olosa amene amatulutsa liwu loti psepsepse ndi kumang'ung'udza.” Kodi anthu sayenera kupempha nzeru kwa milungu yao? Kodi sungapite kwa anthu akufa kukapemphera nzeru anthu amoyo,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang'ung'udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu akakuwuza kuti kafunsire kwa oyankhula ndi mizimu, amene amayankhula monongʼona ndi mongʼungʼudza, kodi anthu sayenera kukafunsira kwa Mulungu wawo? Chifukwa chiyani amafunsira kwa anthu akufa mʼmalo mwa kwa anthu amoyo,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang'ung'udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao? Cifukwa ca amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?