Isaiah 8:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti mwanayo asanayambe kuitana kuti ‘Ababa’ kapena kuti ‘Amama’, chuma cha Damasiko ndi zofunkha za Samariya zidzatengedwa ndi mfumu ya ku Asiriya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa kuti mwana asakhale ndi nzeru yakufuula, Atate wanga, ndi Amai wanga, chuma cha Damasiko ndi chofunkha cha Samariya chidzalandidwa pamaso pa mfumu ya Asiriya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwanayo asanayambe kudziwa kuyitana kuti, ‘Ababa’ kapena ‘Amama’ chuma cha Damasiko ndi zofunkha za Samariya zidzatengedwa ndi mfumu ya ku Asiriya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa kuti mwana asakhale ndi nzeru yakupfuula, Atate wanga, ndi Amai wanga, cuma ca Damasiko ndi cofunkha ca Samariya cidzalandidwa pamaso pa mfumu ya Asuri.