Isaiah 8:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Ine Ambuye ndidzaŵadzetsera mfumu ya ku Asiriya ndi ankhondo ake kuti adzathire nkhondo Yuda. Adzabwera ngati chigumula cha madzi a mtsinje wa Yufurate osefukira pa magombe ake onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake, taonani, Ambuye atengera pa iwo madzi a mtsinje wa Yufurate, olimba ndi ambiri, kunena mfumu ya Asiriya ndi ulemerero wake wonse; ndipo iye adzadzala mphaluka zake zonse, nadzasefukira pamtunda ponse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
nʼchifukwa chake Ambuye ali pafupi kubweretsa madzi amkokomo a mtsinje wa Yufurate kudzalimbana nawo; mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lake lonse lankhondo. Madziwo adzasefukira mʼngalande zake zonse ndi mʼmagombe ake onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace, taonani, Ambuye atengera pa iwo madzi a Nyanja, olimba ndi ambiri, kunena mfumu ya Asuri ndi ulemerero wace wonse; ndipo iye adzadzala mphaluka zace zonse, nadzasefukira pamtunda ponse.