Isaiah 9:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma anthu amene anali ndi nkhaŵa, sadzakhalanso otaya mtima. Masiku amakedzana Mulungu adaanyozetsa dziko la Zebuloni ndi la Nafutali, koma kutsogolo kuno adzalisandutsa laulemu dera lonseli, kuyambira ku nyanja yaikulu kuzambwe mpaka kukafika ku dziko la patsidya pa mtsinje wa Yordani, ndiye kuti dziko la Galilea, dziko la anthu a mitundu ina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kumene kunali nsautso sikudzakhala kuziya. Poyamba paja Mulungu ananyozetsa dziko la Zebuloni, ndi dziko la Nafutali, koma potsiriza pake Iye analichitira ulemu, pa khwalala la kunyanja, patsidya pa Yordani, Galileya wa amitundu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu amene anali ndi nkhawa, sadzakhalanso otaya mtima. Masiku amakedzana Mulungu ananyozetsa dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali, koma kutsogolo kuno dera lonse la Galileya, limene lili dziko la anthu a mitundu ina, kuyambira ku nyanja yayikulu, mʼmbali mwa Yorodani, adzalisandutsa laulemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kumene kunali nsautso sikudzakhala kuziya. Poyamba paja Mulungu ananyozetsa dziko la Zebuloni, ndi dziko la Naftali, koma potsiriza pace Iye analicitira ulemu, pa khwalala la kunyanja, patsidya pa Yordano, Galileya wa amitundu.