Isaiah 9:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asiriya chakuvuma ndi Afilisti chakuzambwe ayasama kukamwa kuti adye Aisraele. Komabe mkwiyo wa Mulungu sudaŵachoke chifukwa cha zonsezi, ndipo mkono wake uli chisamulirecho kufuna kuŵalanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israele ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Asiriya ochokera kummawa ndi Afilisti ochokera kumadzulo ndipo ayasama pakamwa kuti adye a Israeli. Komabe, mkwiyo wake sunawachokere, mkono wake uli chitambasulire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israyeli ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wace sunacoke, koma dzanja lace liri citambasulire.