Isaiah 9:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Ambuye sadzakondwera nawo achinyamata, ndipo sadzaŵachitira chifundo ana amasiye ndi akazi amasiye. Pakuti aliyense ndi wosasamala za Mulungu ndiponso ndi wochimwa. Pakamwa paliponse pamalankhula zopusa. Komabe mkwiyo wa Mulungu sudaŵachoke chifukwa cha zonsezi, ndipo mkono wake uli chisamulirecho kufuna kuŵalanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Ambuye sadzakondwera ndi anyamata ao, ngakhale kuwachitira chifundo amasiye ao ana ndi akazi; popeza yense ali wodetsa ndi wochimwa, m'kamwa monse mulankhula zopusa. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Ambuye adzakondwera nawo achinyamata, ngakhale kuwachitira chifundo ana amasiye ndi akazi amasiye, pakuti aliyense ndi wosapembedza Mulungu ndiponso ndi wochimwa ndipo aliyense amayankhula zopusa. Komabe, mkwiyo wake sunawachokere, mkono wake uli chitambasulire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Ambuye sadzakondwera ndi anyamata ao, ngakhale kuwacitira cifundo amasiye ao ana ndi akazi; popeza yense ali wodetsa ndi wocimwa, m'kamwa monse mulankhula zopusa. Mwa izi zonse mkwiyo wace sunacoke, koma dzanja lace liri citambasulire.