Isaiah 9:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuipa kwa anthuwo kumayaka ngati moto, moto wake wotentha mkandankhuku ndi minga. Umayatsanso nkhalango ndipo utsi wake umachita kuti toloo ngati mtambo wochindikira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti kuchimwa kwayaka ngati moto kumaliza lunguzi ndi minga, inde kuyaka m'nkhalango ya m'thengo, ndipo zifuka chapamwamba, m'mitambo yautsi yochindikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndithu kuyipa kwa anthuwo kumayaka ngati moto; moto wake umanyeketsa mkandankhuku ndi minga, umayatsa nkhalango yowirira, ndipo utsi wake umachita kuti toloo ngati mtambo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti kucimwa kwayaka ngati moto kumariza lunguzi ndi minga, inde kuyaka m'nkhalango ya m'thengo, ndipo zifuka capamwamba, m'mitambo yautsi yocindikira.