Isaiah 9:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake mkwiyo wa Chauta Wamphamvuzonse watentha dziko, ndipo anthu ali ngati nkhuni zosonkhera moto. Palibe munthu wochitira chifundo mbale wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'kukwiya kwa Yehova wa makamu, dziko latenthedwa ndithu, anthunso ali ngati nkhuni; palibe munthu wochitira mbale wake chisoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko lidzatenthedwa ndi ukali wa Yehova Wamphamvuzonse, dziko lidzatenthedwa ndipo anthu adzakhala ngati nkhuni zosonkhera moto; palibe munthu amene adzachitire chifundo mʼbale wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'kukwiya kwa Yehova wa makamu, dziko latenthedwa ndithu, anthunso ali ngati nkhuni; palibe munthu wocitira mbale wace cisoni.