Isaiah 9:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amene ankayenda mumdima aona kuŵala kwakukulu. Amene ankakhala m'dziko la mdima wandiweyani, kuŵala kwaŵaonekera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anthu amene anayenda mumdima, aona kuwala kwakukulu; iwo amene anakhala m'dziko la mthunzi wa imfa, kuwala kwatulukira kwa iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu oyenda mu mdima awona kuwala kwakukulu; kwa iwo okhala mʼdziko la mdima wandiweyani kuwunika kwawafikira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anthu amene anayenda mumdima, aona kuwala kwakukuru; iwo amene anakhala m'dziko la mthunzi wa imfa, kuwala kwaturukira kwa iwo.