Isaiah 9:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amanase akuthira Aefuremu nkhondo, Aefuremu akuthira Amanase nkhondo. Onsewo pamodzi akumenyana ndi Yuda. Komabe mkwiyo wa Mulungu sudaŵachoke chifukwa cha zonsezi, ndipo mkono wake uli chisamulirecho kufuna kuŵalanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Manase adzadya Efuremu; ndi Efuremu adzadya Manase, ndipo iwo pamodzi adzadyana ndi Yuda. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Manase adzadya Efereimu ndipo Efereimu adzadya Manase; onsewa pamodzi adzadya Yuda. Komabe pa zonsezi, mkwiyo wake sunawachokere, mkono wake uli chitambasulire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Manase adzadya Efraimu ndi Efraimu adzadya Manase, ndipo iwo pamodzi adzadyana ndi Yuda. Mwa izi zonse mkwiyo wace sunacoke, koma dzanja lace liri citambasulire.