Isaiah 9:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, mwauchulukitsa mtundu wanu, mwaonjezera kukondwa kwa anthu anu. Iwo akukondwa pamaso panu monga m'mene anthu amakondwera nthaŵi ya masika, monganso m'mene anthu amakondwera pogaŵana zofunkha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu mwachulukitsa mtundu, inu mwaenjezera kukondwa kwao; iwo akondwa pamaso panu monga akondwera m'masika, monga anthu akondwa pogawana zofunkha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mwauchulukitsa mtundu wanu ndipo mwawonjezera chimwemwe chawo. Iwo akukondwa pamaso panu, ngati mmene anthu amakondwera nthawi yokolola, ngatinso mmene anthu amakondwera pamene akugawana zolanda ku nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inu mwacurukitsa mtundu, inu mwaenjezera kukondwa kwao; iwo akondwa pamaso panu monga akondwera m'masika, monga anthu akondwa pogawana zofunkha.