Isaiah 9:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti inu mwathyola goli limene linkaŵalemera, ndodo zimene ankamenyera mapewa ao, ndiponso mikwapulo ya anthu oŵazunza, monga mudaachitira pogonjetsa Amidiyani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti goli la katundu wake, ndi mkunkhu wa paphewa pake, ndodo ya womsautsa, inu mwazithyola monga tsiku la Midiyani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga munachitira pogonjetsa Amidiyani, inu mwathyola goli limene limawalemera, ndodo zimene amamenyera mapewa awo, ndiponso mikwapulo ya anthu owazunza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti gori la katundu wace, ndi mkunkhu wa paphewa pace, ndodo ya womsautsa, inu mwazityola monga tsiku la Midyani.