James 1:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dzuŵa limatuluka nkutentha kwake, ndipo limaumitsa udzu. Duŵa la udzuwo limathothoka, kukongola kwake nkutha. Chomwechonso moyo wa wolemerayo udzazimirira ali pakati pa zochita zake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti latuluka dzuwa ndi kutentha kwake, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duwa lake, ndi ukoma wa maonekedwe ake waonongeka; koteronso wachuma adzafota m'mayendedwe ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti dzuwa limatuluka nʼkutentha kwake, ndipo limafotetsa zomera. Duwa lake limathothoka ndipo kukongola kwake kumatheratu. Momwemonso munthu wachuma adzazimirira ngakhale atamachitabe malonda ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti laturuka dzuwa ndi kutentha kwace, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duwa lace, ndi ukoma wa maonekedwe ace waonongeka; koteronso wacuma adzafota m'mayendedwe ace.