James 1:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake siyani chizoloŵezi chilichonse chonyansa, ndiponso kuipamtima kulikonse. Muŵalandire mofatsa mau amene Mulungu adabzala m'mitima mwanu, pakuti ndiwo angathe kukupulumutsani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho chotsani chizolowezi choyipa ndi khalidwe loyipa pakati panu, ndipo modzichepetsa landirani mawu amene anadzalidwa mwa inu, amene akhoza kukupulumutsani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa ici, mutabvula cinyanso conse ndi cisefukiro ca coipa, landirani ndi cifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu.