James 1:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Malamulo a Mulungu ndi angwiro ndiponso opatsa anthu ufulu. Munthu amene amalandira Malamulowo nkumaŵatsata mosamala, amene samangomva mau nkuŵaiŵala, koma amaŵagwiritsa ntchito, ameneyo Mulungu adzamdalitsa pa zochita zake zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m'kuchita kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma munthu amene amayangʼana mwachidwi lamulo langwiro limene limapatsa ufulu ndi kupitiriza kutero, osayiwala chimene wamva koma kuchita adzadalitsika pa zimene amachita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero cipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakucita nchito, adzakhala wodala m'kucita kwace.