James 1:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m'dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chipembedzo chimene Mulungu Atate athu amachivomereza kuti ndi changwiro ndi chopanda zolakwika ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto awo, ndi kudzisunga bwino kuopa kudetsedwa ndi dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: z kuceza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'cisautso cao, ndi 1 kudzisungira mwini wosacitidwa mawanga ndi dziko lapansi.