James 2:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma kapena wina anganene kuti, “Inuyo muli ndi chikhulupiriro, ineyo ndili ndi ntchito zabwino.” Pamenepo ine nkumuyankha kuti, “Uyesetse kundiwonetsa chikhulupiriro chako chopanda ntchito zakecho, ine ndi ntchito zanga ndikuwonetsa chikhulupiriro changa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma wina akati, Iwe uli nacho chikhulupiriro, ndipo ine ndili nazo ntchito; undionetse ine chikhulupiriro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuonetsa iwe chikhulupiriro changa chotuluka m'ntchito zanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma wina anganene kuti, “Inuyo muli ndi chikhulupiriro koma ine ndili ndi ntchito zabwino.” Onetsani chikhulupiriro chanu chopanda ntchito zabwino ndipo ineyo ndidzakuonetsani chikhulupiriro changa pochita ntchito zabwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma wina akati, Iwe uli naco cikhulupiriro, ndipo ine ndiri nazo nchito; undionetse ine cikhulupiriro cako copanda nchito zako, ndipo ine ndidzakuonetsa iweeikhulupiriro canga coturuka m'nchito zanga.