James 2:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono inu pofuna kusamala kwambiri wovala zokongolayo, mumuuza kuti, “Khalani apa pabwinopa”, mmphaŵi uja nkumuuza kuti, “Iwe, kaimirire apo, kapena dzakhale pansi kumapazi kwangaku.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo mukapenyerera iye wovala chokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe, imauko, kapena, khala pansi pa mpando wa mapazi anga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati musamala kwambiri munthu wovala bwinoyu uja, nʼkumuwuza kuti, “Khalani pa mpando wabwinowu,” koma wosauka uja nʼkumuwuza kuti, “Ima apo,” kapena “Khala pansi pafupi ndi chopondapo mapazi angawa,”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo mukapenyerera iye wobvala cokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe, ima uko, kapena, khala pansi pa mpando wa mapazi anga;