James 2:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma inuyo mwakhala mukumnyoza mmphaŵiyo. Kodi si anthu olemera amene amakupsinjani? Si anthu olemera kodi amene amakukokerani ku mabwalo amilandu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma inu mumanyoza munthu wosauka. Kodi sakusautsani inu achuma, nakukokerani iwowa kumabwalo a milandu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mwakhala mukunyoza amphawi. Kodi si anthu olemerawa amene akukudyerani masuku pamutu? Si anthu amenewa amene amakukokerani ku bwalo la milandu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma inu mumanyoza munthu wosauka. Kodi sakusautsani inu acuma, nakukokerani iwowa ku mabwalo a mirandu?