James 3:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndani mwa inu ali wanzeru ndi womvetsa zinthu? Aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru zimaongoleradi zochita zake zofatsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake mu nzeru yofatsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndani mwa inu amene ndi wanzeru ndi womvetsa zinthu? Mulekeni aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru ndiye zikutsogolera kudzichepetsa kwake ndi zochita zake
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ace abwino nchito zace mu nzeru yofatsa.