James 3:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimodzimodzinso lilime: ndi kachiwalo kakang'ono, komabe limadzitama kuti nkuchita zazikulu. Tangoganizani kukula kwake kwa nkhalango imene ingayatsidwe ndi kalilaŵi kakang'ono ka moto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kotero lilimenso lili chiwalo chaching'ono, ndipo lidzikuzira zazikulu. Taonani, kamoto kakang'ono kayatsa nkhuni zambiri!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Momwemonso, lilime ndi kachiwalo kakangʼono ka thupi koma limadzitama kuti nʼkuchita zikuluzikulu. Tangoganizirani za nkhalango yayikulu imene ingapse ndi kalawi kamoto koyamba mochepa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kotero lilimenso liri ciwalo cacing'ono, ndipo lidzikuzira zazikuru, Taonani, kamoto kakang'ono kayatsa nkhuni zambiri!