James 4:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abale, musamasinjirirana. Wosinjirira mbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo a Mulungu. Koma ukaweruza Malamulo a Mulungu, ndiye kuti sukuchita zimene Malamulowo akunena, ukudziyesa woweruza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wake, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suli wochita lamulo, komatu woweruza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale musamanenane. Aliyense wonenera zoyipa mʼbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo. Pamene muweruza malamulo, ndiye kuti simukusunga malamulowo, koma mukuwaweruza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wace, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suliwocita lamulo, komatu woweruza.