James 4:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mumalakalaka zinthu, koma zimakusoŵani, nchifukwa chake mumapha munthu. Mumasirira zinthu, koma simungathe kuzipeza, nchifukwa chake mumamenyana, nkumachita nkhondo. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulakalaka, ndipo zikusowani; mukupha, nimuchita kaduka, ndipo simukhoza kupeza; mulimbana, nimuchita nkhondo; mulibe kanthu, chifukwa simupempha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mumalakalaka zinthu koma simuzipeza, choncho mumapha. Mumasirira zinthu koma simutha kuzipeza zimene mukufuna, choncho mumakangana ndi kumenyana. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulakalaka, ndipo zikusowani; mukupha, nimucita kaduka, ndipo simukhoza kupeza; mulimbana, nimucita nkhondo; mulibe kanthu, cifukwa simupempha.