James 4:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo Iye adzayandikira kwa inu. Muzisamba m'manja, inu anthu ochimwa. Chotsani maganizo onyenga m'mitima mwanu, inu anthu okayikakayika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sendezani kufupi ndi Mulungu ndipo Iye adzasendeza kwa inu. Sambani mʼmanja mwanu, inu anthu ochimwa. Yeretsani mitima yanu, inu anthu okayikira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu, Sambani m'manja, ocimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.