James 5:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho, ululiranani machimo anu ndi kupemphererana wina ndi mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama ndi lamphamvu ndipo limagwira ntchito.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace mubvomerezane wina ndi mnzace macimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzace kuti muciritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukuru m'macitidweace.