James 5:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Eliya anali munthu monga ife tomwe. Iye uja adaapemphera kolimba kuti mvula isagwe, ndipo mvula siidagwedi pa zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera chipempherere kuti isavumbe mvula; ndipo siinagwa mvula pa dziko zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Eliya anali munthu ngati ife. Iye anapemphera mwamphamvu kuti mvula isagwe ndipo sinagwedi kwa zaka zitatu ndi theka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera cipempherere kuti isabvumbe mvula; ndipo, siinagwa mvula pa dzikozaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi.