James 5:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
dziŵani kuti amene adzabweza munthu wochimwa ku njira yake yosokera, adzapulumutsa moyo wa munthuyo ku imfa, ndipo chifukwa cha iye machimo ochuluka adzakhululukidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
azindikire, kuti iye amene abweza wochimwa kunjira yake yosochera adzapulumutsa munthu kwa imfa, ndipo adzavundikira machimo aunyinji.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kumbukirani izi: Aliyense wobweza wochimwa kuchoka ku cholakwa chake, adzamupulumutsa ku imfa ndi kukwirira machimo ambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
azindikire, kuti iyeamene abweza wocimwa ku njira yace yosocera adzapulumutsa munthu kwa imfa, ndipo adzabvundikira macimo aunyinji.