James 5:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Golide wanu ndi siliva zachita dzimbiri, ndipo dzimbirilo lidzakhala mboni yokutsutsani. Lidzaononga thupi lanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano amene ali otsiriza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Golide wanu ndi siliva wanu zachita dzimbiri, ndipo dzimbiri lake lidzachita mboni zoneneza inu, ndipo zidzadya nyama yanu ngati moto. Mwadzikundikira chuma masiku otsiriza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Golide ndi siliva wanu zachita dzimbiri. Dzimbirilo lidzakhala umboni wokutsutsani ndi kuwononga mnofu wanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano otsiriza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Golidi wanu ndi siliva wanu zacita dzimbiri, ndipo dzimbiri lace lidzacita mboni zoneneza Inu ndipo zidzadya nyama yanu ngat: moto. Mwadzikundikira cuma masiku otsiriza.