James 5:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono abale, khazikani mtima pansi mpaka Ambuye adzabwere. Onani m'mene amachitira mlimi. Amadikira kuti zipatso zokoma ziwoneke m'munda mwake. Amangoyembekeza mokhazika mtima kuti zilandire mvula yachizimalupsa ndi yachikokololansanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwake kwa Ambuye. Taonani, wolima munda alindira chipatso chofunikatu cha dziko, ndi kuleza mtima nacho kufikira chikalandira mvula ya chizimalupsa ndi masika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono abale, pirirani mpaka kubwera kwa Ambuye. Onani mmene amachitira mlimi. Amadikirira kuti zipatso zabwino zioneke mʼmunda mwake. Amayembekezera mokhazikika mtima kuyambira nthawi ya mvula yoyamba mpaka yotsiriza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwace kwa Ambuye. Taonani, wolima munda alindira cipatso cofunikatu ca dziko, ndi kuleza mtima naco kufikira cikalandira mvula ya myundo ndi masika,