Jeremiah 1:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikukuika lero kuti ukhale ndi ulamuliro pa maiko a anthu ndi maufumu ao, kuti uzule ndi kugwetsa, kuti uwononge ndi kugumula, kuti umange ndi kubzala.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
penyatu, lero ndakuika ulamulire mitundu ya anthu ndi maufumu, kuti uzule, upasule, uononge, ugwetse, umange, ubzale.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lero ndakusankha kuti ukhale ndi ulamuliro pa mitundu ya anthu ndi pa maufumu awo kuti uzule ndi kugwetsa, uwononge ndi kugumula, kuti uwamange ndi kudzala.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
penyatu, lero ndakuika ulamulire mitundu ya anthu ndi maufumu, kuti uzule, upasule, uononge, ugwetse; umange, ubzyale.