Jeremiah 1:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adandifunsa kuti, “Yeremiya, kodi ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona nthambi ya mtowo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, Yeremiya, uona chiyani? Ndipo ndinati, Ine ndiona nthyole ya katungurume.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anandifunsa kuti, “Yeremiya, kodi ukuona chiyani?” Ine ndinayankha kuti, “Ndikuona nthambi ya mtengo wa mtowo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, Yeremiya, uona ciani? Ndipo ndinati, Ine ndiona ntyole ya katungurume.