Jeremiah 1:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adandifunsa kachiŵiri kuti, “Kodi ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona mbiya yogaduka, yafulatira kumpoto.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yachiwiri, kuti, Uona chiyani? Ndipo ndinati, Ine ndiona mphika wogaduka; ndi pakamwa pake unafulatira kumpoto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anandifunsanso kachiwiri kuti, “Kodi ukuona chiyani?” Ine ndinayankha kuti, “Ndikuona mʼphika wa madzi owira, ndipo wagudukira kuno kummwera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yaciwiri, kuti, ona ciani? Ndipo ndinati, Ine ndiona mphika wogaduka; ndi pakamwa pace unafulatira kumpoto.