Jeremiah 1:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikuitana anthu a mafuko onse a maufumu akumpoto,” akuterotu Chauta. “Mafumu ao adzabwera, aliyense adzaika mpando wake waufumu pa zipata za Yerusalemu, ndiponso pozungulira malinga ake. Iwo adzazinganso mizinda yonse ya Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti taona, ndidzaitana mabanja onse a maufumu a kumpoto, ati Yehova; ndipo adzafika nadzaika yense mpando wachifumu wake pa zipata za Yerusalemu, ndi pa malinga onse ozinga pamenepo, ndi pa midzi yonse ya Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndikuyitana anthu onse a ku maufumu a kumpoto,” akutero Yehova. “Mafumu awo adzabwera ndipo aliyense adzakhazika mpando wake waufumu polowera pa zipata za Yerusalemu; iwo adzabwera ndi kuzungulira makoma ake ndiponso midzi yonse ya dziko la Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti, taona, ndidzaitana mabanja onse a maufumu a kumpoto, ati Yehova; ndipo adzafika nadzaika yense mpando wacifumu wace pa zipata za Yerusalemu, ndi pa malinga onse ozinga pamenepo, ndi pa midzi yonse ya Yuda.