Jeremiah 1:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzatulutsa mlandu wanga wotsutsa anthu anga, chifukwa cha zoipa zimene adachita pakundisiya Ine. Adafukiza lubani kwa milungu ina, namapembedza zimene adapanga ndi manja ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzanena nao za maweruzo anga akuweruzira zoipa zao zonse; popeza anandisiya Ine, nafukizira milungu ina, nagwadira ntchito za manja ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzatulutsa mlandu wanga ndi iwo chifukwa cha zoyipa zimene anachita pondisiya Ine. Iwo anakafukiza lubani kwa milungu ina, ndi kupembedza zimene anapanga ndi manja awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzanena nao za maweruzo anga akuweruzira zoipa zao zonse; popeza anandisiya Ine, nafukizira milungu yina, nagwadira nchito za manja ao.