Jeremiah 1:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Lero ine ndikukulimbitsa ngati mzinda wamalinga, mzati wachitsulo, ndiponso ngati makoma amkuŵa, kuti usachite mantha ndi wina aliyense m'dziko lonse, kaya ndi mafumu a ku Yuda, nduna zakumeneko, ansembe kapena anthu wamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa, taona, ndakuyesa iwe lero mudzi walinga, mzati wachitsulo, makoma amkuwa, pa dziko lonse, ndi pa mafumu a Yuda, ndi pa akulu ake, ndi pa ansembe ake, ndi pa anthu a m'dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taona, lero ndakupanga kukhala ngati mzinda wotetezedwa, ngati mzati wachitsulo ndiponso ngati makoma a mkuwa kuti usaopsedwe ndi munthu aliyense wa mʼdzikomo; kaya ndi mafumu a Yuda, akuluakulu ake, ansembe ake, kapena munthu wamba wa mʼdzikomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa, taona, ndakuyesa iwe lero mudzi walinga, mzati wacitsulo, makoma amkuwa, pa dziko lonse, ndi pa mafumu a Yuda, ndi pa akuru ace, ndi pa ansembe ace, ndi pa anthu a m'dziko.