Jeremiah 1:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adalankhula nayenso pa nthaŵi ya Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, mpaka mwezi wachisanu wa chaka cha khumi ndi chimodzi cha Zedekiya, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, pamene anthu a ku Yerusalemu adatengedwa ukapolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anamdzeranso masiku a Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kufikira Zedekiya mwana wake wa Yosiya mfumu ya Yuda atatsiriza zaka khumi ndi chimodzi; kufikira a ku Yerusalemu anatengedwa ndende mwezi wachisanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anayankhulanso naye pa nthawi yonse ya ulamuliro wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, mpaka mwezi wachisanu wa chaka cha 11 cha ufumu wa Zedekiya mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, pamene anthu a ku Yerusalemu anapita ku ukapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anamdzeranso masiku a Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kufikira Zedekiya mwana wace wa Yosiya mfumu ya Yuda atatsiriza zaka khumi ndi cimodzi; kufikira a ku Yerusalemu anatengedwa ndende mwezi wacisanu.