Jeremiah 10:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ali apa amvekere, “Kalanga ine chifukwa cha kupweteka koopsa! Bala langa ndi lomvetsa chisoni. Kale ndinkati chimenechi ndi chilango changa, ndingochipirira basi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka ine, ndalaswa! Bala langa lindipweteka; koma ine ndinati, Ndithu vuto langa ndi ili, ndipirire nalo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense ankangoti, “Mayo ine, chifukwa cha kupweteka kwanga! Chilonda changa nʼchachikulu!” Koma ine ndinkaganiza kuti, “Ndithu, ili ndi vuto langa basi, choncho ndingolipirira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka ine, ndalaswa! bala langa lindipweteka; koma ine ndinati, Ndithu bvuto langa ndi ili, ndipirire nalo.