Jeremiah 10:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Hema langa laonongeka, zingwe zake zonse zaduka. Ana anga andisiya ndipo kulibenso. Palibenso wina woti nkundikhomera hema, kapena woti nkufunyulula nsalu zake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Hema wanga waonongeka, zingwe zanga zonse zaduka; ana anga atuluka mwa ine, palibe iwo; palibenso amene adzamanga hema wanga, kapena kutchinga nsalu zanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tenti yanga yawonongeka, zingwe zake zonse zaduka. Ana anga andisiya ndipo kulibenso. Palibenso amene adzandimangire tenti, kapena kufunyulula nsalu yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Hema wanga waonongeka, zingwe zanga zonse zaduka; ana anga aturuka mwa ine, palibe iwo; palibenso amene adzamanga hema wanga, kapena kucinga nsaru zanga,