Jeremiah 10:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tamvani, kukubwera mphekesera. Kumpoto kukuchokera chinamtindi chosokosa chodzasakaza mizinda ya Yuda, kuti isanduke bwinja, mokhala nkhandwe basi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mbiri yamveka, taonani ikudza, ndi phokoso lalikulu lituluka m'dziko la kumpoto, likachititse midzi ya Yuda bwinja, ndi mbuto ya nkhandwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tamvani! kukubwera mphekesera, phokoso lalikulu la gulu la a ankhondo likumveka kuchokera kumpoto! Lidzasandutsa bwinja mizinda ya ku Yuda, malo okhala nkhandwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mbiri yamveka, taonani ikudza, ndi phokoso lalikuru lituruka m'dziko la kumpoto, likacititse midzi ya Yuda bwinja, ndi mbuto ya nkhandwe.