Jeremiah 10:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ukali wanu uyakire mitundu imene sikudziŵani, ndiye kuti anthu amene satama dzina lanu mopemba. Iwo adasakaza anthu anu ndi kuŵaononga kotheratu ndipo dziko lao adalisandutsa bwinja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsanulirani ukali wanu pa amitundu osakudziwani Inu, ndi pa mabanja osaitana dzina lanu; pakuti anadya Yakobo, inde, anamudya namutha, napasula mokhalamo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsanulirani ukali wanu pa mitundu ya anthu amene sakudziwani, ndiye kuti mitundu ya anthu amene satama pa dzina lanu mopemba. Iwo aja anasakaza Yakobo; amusakaza kotheratu ndipo awononga dziko lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsanulirani ukali wanu pa amitundu osakudziwani Inu, ndi pa mabanja osaitana dzina lanu; pakuti anadya Yakobo, inde, anamudya namutha, napasula mokhalamo mwace.