Jeremiah 10:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndithudi, miyambo ya anthu a mitundu inayo nzopanda pake. Iwo aja amakadula mtengo ku nkhalango, munthu waluso namausema ndi nsompho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti miyambo ya anthu ili yachabe, pakuti wina adula mtengo m'nkhalango, ntchito ya manja a mmisiri ndi nkhwangwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti miyambo ya mitundu inayo ndiyachabechabe. Iwo amakadula mtengo ku nkhalango ndipo mmisiri amawusema ndi sompho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti miyambo ya anthu iri yacabe, pakuti wina adula mtengo m'nkhalango, nchito ya manja a mmisiri ndinkhwangwa.