Jeremiah 10:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ena amakongoletsa chosemacho ndi siliva ndi golide, kenaka nkuchikhomerera ndi misomali, kuti chisagwedezeke.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Aukometsa ndi siliva ndi golide; auchirikiza ndi misomali ndi nyundo, kuti usasunthike.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amakongoletsa chosemacho ndi siliva ndi golide; kenaka amachikhomerera ndi misomali kuti chisagwedezeke.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Aukometsa ndi siliva ndi golidi; aucirikiza ndi misomali ndi nyundo, kuti usasunthike.