Jeremiah 10:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mafano aowo ali ngati kangamunthu woopsera mbalame m'munda wa minkhaka, sangathe nkulankhula komwe. Ayenera kuŵanyamula, poti sangayende okha. Musaŵaope, chifukwa sangakuchiteni choipa. Alibenso mphamvu zochitira zabwino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mafanowa akunga mtengo wakanjedza, wosemasema, koma osalankhula; ayenera awanyamule, pakuti sangathe kuyenda. Musawaope; pakuti sangathe kuchita choipa, mulibenso mwa iwo kuchita chabwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mafano awo ali ngati mtengo wakanjedza woopsezera mbalame mʼmunda wa minkhaka. Mafanowo sangathe nʼkuyankhula komwe ndipo ayenera kunyamulidwa popeza sangathe nʼkuyenda komwe. Musachite nawo mantha popeza sangathe kukuchitani choyipa ndiponso alibe mphamvu yochitira chabwino chilichonse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mafanowa akunga mtengo wakanjedza, wosemasema, koma osalankhula; ayenera awanyamule, pakuti sangathe kuyenda. Musawaope; pakuti sangathe kucita coipa, mulibenso mwa iwo kucita cabwino.