Jeremiah 10:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Siliva wosula wokutira mafanowo ndi wochokera ku Tarisisi, ndipo golide wake ndi wochokera ku Ufazi. Mafano aowo ndi ntchito ya anthu aluso ndi anthu odziŵa kuzokota golide. Amaveka mafanowo nsalu zonyezimira ndi zofiirira. Zonsezo ndi ntchito ya anthu aluso chabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Abwera ndi siliva wa ku Tarisisi, wosulasula wopyapyala ndi golide wa ku Ufazi, ntchito ya mmisiri ndi manja a woyenga; zovala zao ndi nsalu ya madzi ndi yofiirira; zonsezi ndi ntchito za muomba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Siliva wosula amabwera naye kuchokera ku Tarisisi ndipo golide amachokera naye ku Ufazi. Mafanowo ndi ntchito ya anthu aluso ndi odziwa kuzokota golide. Tsono mafanowo amawaveka zovala za mtundu wamtambo ndi pepo. Yonseyo ndi ntchito ya anthu a luso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Abwera ndi siliva wa ku Tarisi, wosulasula wopyapyala ndi golidi wa ku Ufazi, nchito ya mmisiri ndi manja a woyenga; zobvala zao ndi nsaru ya madzi ndi yofiirira; zonsezi ndi nci ito za muomba.