Jeremiah 11:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abwereranso ku machimo a makolo ao amene adakana kundimvera. Akutsata milungu ina ndi kumaipembedza. A ku Israele ndi a ku Yuda aphwanya chipangano chimene ndidapangana ndi makolo ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Abwerera kuchitanso zoipa za makolo ao, amene anakana kumva mau anga; ndipo atsata milungu ina kuti aitumikire; nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda zaswa pangano langa limene ndinapangana ndi makolo ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abwereranso ku machimo a makolo awo, amene anakana kumvera mawu anga. Akutsata milungu ina ndi kumayitumikira. Aisraeli ndi Ayuda aphwanya pangano limene ndinachita ndi makolo awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Abwerera kucitanso zoipa za makolo ao, amene anakana kumva mau anga; ndipo atsata milungu yina kuti aitumikire; nyumba ya Israyeli ndi nyumba ya Yuda zaswa pangano langa limene ndinapangana ndi makolo ao.