Jeremiah 11:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a m'mizinda ya ku Yuda ndi a mu Yerusalemu adzapita kukalirira chithandizo kwa milungu imene ankaperekako nsembe. Koma singathe kuŵapulumutsa pa nthaŵi ya mavuto ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo midzi ya Yuda ndi okhala m'Yerusalemu adzapita nadzafuulira kwa milungu imene anaifukizira; koma siidzawapulumutsa konse nthawi ya nsautso yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a mʼmizinda ya Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu adzapita ndi kukalirira milungu imene ankayifukizira lubani, koma milunguyo sidzawathandiza ndi pangʼono pomwe mavuto akadzafika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo midzi ya Yuda ndi okhala m'Yerusalemu adzapita nadzapfuulira kwa milungu imene anaifukizira; koma siidzawapulumutsa konse nthawi ya nsautso yao.