Jeremiah 11:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zoonadi, iwe Yuda, milungu yako yachuluka ngati chiŵerengero cha midzi yako. Maguwa ootcherapo nsembe kwa Baala achuluka ngati miseu ya mu Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti milungu yako ilingana ndi kuchuluka kwa midzi yako, iwe Yuda; ndi maguwa a nsembe amene mwautsira chamanyazi, alingana ndi kuchuluka kwa miseu ya Yerusalemu, ndiwo maguwa akufukizirapo Baala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe Yuda, uli ndi milungu yochuluka ngati chiwerengero cha mizinda yako; chiwerengero cha maguwa ansembe amene umafukizirapo lubani kwa Baala chili ngati misewu ya mu Yerusalemu.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti milungu yako ilingana ndi kucuruka kwa midzi yako, iwe Yuda; ndi maguwa a nsembe amene mwautsira camanyazi, alingana ndi kucuruka kwa miseu ya Yerusalemu, ndiwo maguwa akufukizirapo Baala.