Jeremiah 11:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono iwe Yeremiya, usaŵapempherere anthu ameneŵa. Usaŵapepesere kwa Ine kapena kuŵadandaulira. Ndithu, Ine sindidzaŵamvera akadzandiitana pa nthaŵi ya mavuto ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake usawapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu, kapena pemphero, pakuti sindidzamva iwo nthawi imene andifuulira Ine m'kusauka kwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono iwe Yeremiya usawapempherere anthu amenewa ngakhale kuwadandaulira kapena kuwapepesera, chifukwa sindidzawamvera akadzandiyitana pa nthawi ya mavuto awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace usawapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu, kapena pemphero, pakuti sindidzamva iwo nthawi imene andipfuulira Ine m'kusaukakwao.