Jeremiah 11:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi anthu anga okondedwa adzachitanji m'Nyumba mwanga? Suja iwowo achita zoipa kwambiri? Kodi malumbiro anu ndi nyama zopereka ku nsembe zingathe kukutetezani ku tsoka lanu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wokondedwa wanga afunanji m'nyumba mwanga, popeza wachita choipa ndi ambiri, ndipo thupi lopatulika lakuchokera iwe? Pamene uchita choipa ukondwera nacho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi anthu anga okondedwa akudzachita chiyani mʼNyumba yanga? Kodi suja iwowa amachita zoyipa zambiri? Kodi mungathe kupulumuka, tsoka osakugwerani chifukwa cha nsembe zanuzo?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wokondedwa wanga afunanji m'nyumba mwanga, popeza wacita coipa ndi ambiri, ndipo thupi lopatulika lakucokera iwe? pamene ucita coipa ukondwera naco.